About

Dera langa

Ndi njira yoyendetsedwa ndi nzika yokonzedwa kuti ilimbikitse mawu a nzika wamba pa chitukuko ndi  utsogoleri wa m’madera kuno Malawi. Nsanja yathu imalola anthu ochokera m’madera onse kutumiza mafunso, madandaulo, kapena malipoti okhudza mavuto a m’madera — ndipo imatsimikizira kuti nkhawa zimenezi zifika kwa akuluakulu oyenerera a makhonsolo awo.

Cholinga Chathu 


Cholinga chathu ndi kulimbikitsa kuonekera poyera, kuyankha mwachangu, komanso kutenga nawo mbali kwa anthu a m’madera kudzera pa makina a internet otetezeka komaso opereka mphamvu kwa anthu kuti apereke ma madando mopanda mantha. Tikukhulupirira kuti nzika zomwe zimalimbikitsidwa kulumikizana ndi adindo awo zimapanga madera abwino komaso otukuka.

Amene Timagwira Nawo Ntchito  


Timagwirizana ndi ma khonsolo a m’madera a dziko lino kufuna  kuthandiza nzika kuti zitumize komaso ziyankhidwe madando ochokera madera awo. 

Gulu Lathu


Gulu lathu lili ndi  akatswiri pa uthenga wa chituko, akaswiri opanga  masamba a internet komaso nthumwi za mu ma khonsolo.  onse odzipereka kuti kulumikizana kwa nzika kukhale kosavuta komanso kogwira ntchito bwino.

Our Values / Makhalidwe Athu

  • Transparency (Kuwonekera bwino)

  • Respect (Ulemu)

  • Responsiveness (Kuyankha Mofulumira)

  • Non-partisanship (Opanda tsankho wa ndale)

  • Empowerment (Kulimbikitsa nzika)

  • Participatory communication ( Kulumikizana mwa umodzi)
  • Honesty ( kukhulupilika)